Mutharika apambana ndi 58%

…Chakwera apeza 33.5%

The Investigator Magazine itha kulengeza tsopano kuti mtsogoleri wakale wa dziko la Malawi a Peter Mutharika apambana chisankho cha udindo wa President ndi ma vote pafupi fupi 2.8 million yomwe ndi 58% ya anthu pafupi 4.8 million omwe anatenga nawo gawo pa zisankho za chaka chino.

Owatsatila ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Dr. Lazarus Chakwera omwe apeze mavoti osapitilila 1.7 million, yomwe ndi 33.5% ya anthu omwe aponia vote.

Professor Peter Mutharika amayimila chipani cha DPP ndipo chipanichi chikutsogolanso pa mipando ya aphungu a nyumba ya malamulo, ngakhale omwe achuluke akhale oyima pawokha (independents).

Kuyambila pomwe voti inatsekedwa, tinayika anthu mboma lililonse kuti ajambule zotsatila zomwe zayikidwa panja pa malo ovotela, ndipo pamene timamaliza kolemba nkhaniyi ndiye kuti kwatsala madela 11 okha a phungu a ku nyumba ya malamulo kuti tipeze ma form ovomelezeka pa ma centre awo onse.

Professor Mutharika achita bwino chigawo cha kummwera komwe Dr. Chakwera akutsalira kwambiri. President Chakwera wachita bwino chigawo cha pakati koma a Mutharika nawo akupeza mavoti ochuluka mmaboma ngati Salima, Nkhotakota, mu mzinda wa Lilongwe ndi Kasungu.

Chipani cha DPP chapeza aphungu ku Kasungu, Salima ndi Lilongwe pomwe MCP yapeza phungu mmodzi chigawo cha ku mmwela a Steven Gerlad ku Mangochi Makanjira.

Bungwe loyendetsa za chisankho likuyenela kulengeza zotsatilazi koma nyumba zambiri zowulutsila mau nazonso zikuonetsa kuti a Mutharika apambana.

a Mutharika kuoneka kuti akutsogola Source: https://lunthaelections.com/

The Investigator Magazine inayika ma vote omwe imayembekezela mmaboma onse ndipo maboma ambiri zotsatila zikugwirizana ndi kafukufuku wathu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *