MEC iyamba kukonzekera zisankho  za 2025

….A Chilima akuzadziwa ngati akudzayima pa 18 Juni, 2025

…Nyumba ya Malamulo ikudzayimitsidwa pa 16 Juni, 2025

…Kalembera wapadera achitika mu Novembala

Nthawi yokonzekera chisankho cha mu 2025 yayambika pamene bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) likukonza zoyamba kusanthula ndi kuvomereza nthumwi zogwira nawo ntchito mwezi uno komanso kuchititsa kalembera woyeserera mu mwezi wa Novembala chaka chino. 

Bungwe la MEC linakhazikitsa ndondomeko yake yogwirira ntchito ndinso ndondomeko yoyendetsera chisankho yomwe ikuwonetsa kuti zipani za ndale ndinso nthumwi zina nthawi yawathera yosonkhanitsa pamodzi anthu awo odzayang’anira komanso kukonzekera chisankho chikubwerachi.

Pulezidenti Lazarus Chakwera, wachiwiri wake a Saulos Chilima, aphungu ndi makhansala angotsala ndi miyezi yosachepera isanu ndi inayi (9) ku nthawi yomwe bungwe la MEC ikuyembekezeka kudzakhazikitsa nthawi ya zokonzekera za chisankho mu mwezi wa Meyi 2024 ndipo idzatsatizana ndi kuthetsedwa kwa Nyumba ya Malamulo yomwe inali ndi materemu asanu ndi imodzi mchaka chobweracho.

Malingana ndi bungweli, onse omwe akufuna kudzapanga nawo ntchito yophunzitsa anthu za chisankho akuyenera kudzapereka makalata awo bungweli likadzayitanitsa zikalatazi mwezi uno kapena wa mawa, pomwe pa 1 Novembala, zipani zikuyenera kudzakhala ndi ma monitala wodzayang’anira kalembera woyeserera.

Kuyamba ntchito mu 2023

Kwa zipani za ndale, ofuna kudzapikisana nawo ndinso nthumwi zina, zambiri mwa zokonzekera zomwe zikuchitika zayenera kukhala zowapatsa chidwi chifukwa kutsatira bwino ndondomeko ya zochitika ndizofunikira kwambiri kwa omwe akufuna kudzapambana. 

Bungwe la MEC lamaliza kale ntchito yogawanso ndi kutsimikiza madera atsopano a aphungu kotero pamene limakhazikitsa ndondomeko yogwirira ntchito komanso ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankho ku Lilongwe, ilo linali litayamba kale kubweretsa dziko lino chifupi ku chisankhochi chomwe chatsala miyezi 24.

Kupatula madera a aphungu atsopano, bungwe la MEC lasayina kale mgwirizano ndi nthambi yoona za kalembera wa unzika la National Registration Bureau (NRB) ndinso kuvomerezedwa ndi Nyumba ya Malamulo kwa malamulo atsopano a chisankho kuphatikizapo la 50 + 1 pa chisankho cha pulezidenti.

Zina mwa ntchito mchakachi zinali monga mikumano ndi nthumwi zosiyanasiyana pa dongosolo la kalembera, kutsindikiza malire a madera a aphungu ndi makhansala a chisankho cha 2025, kudziwitsa anthu za madongosolo ena a chisankho.

Mkumano winanso wa National Elections Consultative Forum pa nkhani ya malire atsopano ndi malo ena umayenera kuchitika kale pomwe kwa omwe akufuna kudzachita nawo kuphunzitsa athu za chisankho akuyenera kukhala tcheru chifukwa bungweli likuyembekezeka kudzalengeza kuti ofuna atumize makalata awo chaka chomwe chino.

Kalembera woyeserera akuyembekezeka kuchitika mwezi wonse wa Novembala ndi iyi idzakhala ntchito yomaliza mchaka cha 2023 pokonzekera chisankho cha 2025.

Kukonzekera mu 2024 

Bungwe la MEC lidzagwiritsa ntchito miyezi iwiri yoyambirira kapena isanu yakumayambiriro mchaka cha 2024 kudziwitsa nthumwi za chisankho za malamulo atsopano ndipo kumapeto kwa mwezi wa Febuluwale adzalengeza omwe akuyembekezeka kupanga ntchito yophunzitsa anthu. Ilo likuyembekezanso kudzakhazikitsa kaundula wa chisankho cha mu 2025 pa 16 Meyi, 2024 motsogozana ndi msonkhano wa atolankhani ndinso ndondomeko yophunzitsira anthu za chisankhochi.

A Chilima akuzadziwa ngati akudzayima pa 18 Juni, 2025

Mu mwezi wa Julaye nthumwi zoyan’ganira chisankho zakunja zizidzalandira makala owayitana pomwe nthumwi za m’maboma nazonso zizidzalandira katundu wina ndi wina kutsatizana ndi mikumano ya mafumu akuluakulu. Pa 26 Julaye, 2024 bungwe la MEC likuyembekezeka kudzatsindikiza nthawi ya kalembera ndipo zipani ndi oyang’anira chisankho akuyenera kudzapereka mayina a anthu awo kumapeto kwa mwezi wa Ogasiti ndicholinga choti adzayang’anire ntchito ya kalembera.

Ogasiti ukuyembekezeka kudzakhalanso mwezi wa zochitika zambiri kaamba koti ndi mwezi omwe zipangizo zina ndi zina zitadzayambe kugawidwa, kukhazikitsa kwa ndondomeko ya momwe atolankhani akuyenera kudzagwirira ntchito komanso mikumano ina ndi ina monga ya NECOF. Mu mwezi womwewu chipani cha MCP chikudzakhala ndi msonkhano wake waukulu.

Mtsogoleri wakale wa dziko la Malawi, His Excellency Prof Peter Muthalika kodi aima nawo?

Bungweli likuyembekezanso kudzayamba kumema anthu kuti akalembetse kutatsala chaka chimodzi anthu asanakavote pa 16 Sepitembala, 2024 ndipo kalembera wa ovota akuyembekezeka kudzachitika mmagawo asanu ndi limodzi (6). Odzapikisana nawo akuyembekezeka kuzadziwa ndalama zomwe akuyenera kudzalipira ku bungweli pofika pa 1 Novembala, 2024.

Kusankha atsogoleri atsopano

Bajeti ya boma la mgwirizano wa Tonse ikuyenera kudzaperekedwa kumayambiro a 2025 koma pa nthawiyi nkuti zina ndi zina zokhudza chisankho zitayamba mu Janyuwale monga mikumano ya kaundula wa kalembera. 

Kuchokera pa 3 mpaka 9 Febuluwale, ovota atha kumadzasintha komwe akufuna kudzavotera, mikumano pa kaundula wa ovota, kusankhidwa kwa odzayimira oa chisankho komanso kuyendera kaundula wa kalembera wa ovota zikuyembekezeka kudzachitika pakati pa Febuluwale ndi Epulo.

Pa 10 Epulo, MEC ikuyembekezeka kudzalengeza chidziwitso cha kaperekedwe ka zikalata za oyimira zipani pa tiketi ya pulezidenti, phungu ndi khansala ndipo izi zidzatero mpaka pa 9 Meyi komanso kutengedwa kwa zikalata za chisankho cha makhansala kuchokera ku ma ofesi a bwanamkubwa kwa oyimira.Odzapikisana nawo pa mpando wa uphungu akuyembekezeka kudzatenga makalata awo 10 Epulo mpaka pa 13 Juni pomwe odzayimira pa mpando wa pulezidenti akuyenera kudzapita ku maofesi a bungwe la MEC konko.

Pa 18 Epulo ndi tsiku lomwe lakonzedwa ngati lophunzitsa anthu za chisankho pomwe pa 24 ndi MEC ikudzayenera kulengeza kuyamba kugwira ntchito kwa madera a aphungu ndi makhansala atsopano.

Odzayimira pa ukhansala akudzayenera kupereka makalata awo ku malo owerengera mavoti aku dera (constituency tally centre) kuyambira pa 5 mpaka 9 Meyi ndipo pa 23 Meyi MEC idzalengeza mndandanda wa odzayimira. Kumbali ya ma pulezidenti, iwo adzakapereka makalata awo pa 11 mpaka 13 Juni pamene a Chilima omwe akuyembekezeka kudzayimira UTM akuyenera kudzadikira pa 18 Juni 2025 kuti adzamve ngati MEC ingadzawalole kuyimanso chifukwa pali mafunso ambiri ngati iwo ndiwoyenera kudzayima kapena ayi potengera ndi zoti iwo atumikira kale ma teremu awiri. 

Zipani zikuyenera kukhala ndi mwayi wowunika mapepala odzaponyera voti pakati pa 3 ndi 8 Julayi  ndipo nthawi ya misonkhano yokopa anthu ikuyembekezeka kudzakhazikitsidwa pa 15 Julayi ndipo pa 25 Julayi mpaka kumapeto kwa mwezi wa Sepitembala zipani zitha kudzawunika kakonzedwe ka mapepala odzavotera komanso omadzalembapo zotsatira. Mapepala odzaponyera voti adzadindidwa pa 1 Ogasiti mpaka 31 Ogasiti ndipo iyi ndi nthawi yomwenso bungweli lizidzapangitsa maphunziro apadera a odzayendetsa chisankho. 

Kamuthemuthe

Mapepala odzaponyera voti akuyenera kudzafika mdziko muno pakati pa 5 ndi 7 Seputembala ndipo kutumizidwa mmadera kudzayamba pa 10 kwa masiku awiri. Malo ovotera adzayamba kulandira zipangizo zodzavotera pa 13 mpaka pa 14 Seputembala. Nthawi yotseka misonkhano yotseka anthu idzakhala 6 kololo mmawa pa 14 Seputembala pamene pa 15 lidzakhala tsiku lowona zipangizo zodzavotera ngati zili mchimake ndipo izi zidzachitika kuchokera pa 9 koloko mmawa mpaka 11 koloko mmawanso.  Pa 15 ndipomwenso patadzakhalenso maphunziro apadera othandizira kuyendetsa chisankho ndipo pa 16 Seputembala ndipomwe Amalawi akuyembekezeka kudzasankhanso atsogoleri atsopano.

Zotsatira za pulezidenti zikuyembekezeka kudzatulutsidwa pa 24 Seputembala, aphungu pa 30 ndipo makhansala pa 7 Okutobala.

Pakadali pano, tapeza kuti zokambitrana zili mkati pakati pa a ndale, aphunzitsi aku sukulu za ukachenjede komanso ena pa kupeza munthu wamphamvu woti atha kudzayimira nawo pa mpando wa pulezidenti kaamba koti anthu sakukondwa ndi omwe akufuna kudzayimira panowa.

Mwa maina omwe akumveka kuti atha kudzatsogolera mgwirizano wina ndi monga Stanley Onjezani Kenani, Bishopu Martin Mtumbuka, mtsogoleri wakale a Joyce Banda, Thom Mpinganjira, Simbi Phiri ndi a Napoleaon Dzombe

Ndondomeko wa zochitika mpaka Chisankho

August 2023 :                  Kuyamba kusanthula mabungwe ophunzitsa za chisankho

Novembela 2023:             Kalembera woyeserera

Febuluwale 2024:              Kutsindikiza mndamndanda wa odzaphunzitsa anthu  za chisankho

Meyi 16, 2024    :               Msonkhano wa atolankhani pa kukhazikitsa za chisankho chachikulu cha mu 2025 

Julayi 1, 2024        :               Kutumiza makalata oyitana odzayang’anira chisankho

Ogasiti 2024      :               Kupereka mayina a oyimira zipani pa kalembera wa ovota

Seputembala 16, 24 :       Kalembera wa ovota m’magawo asanu limodzi (6)   

Novembela 1       :               Kulengeza kwa ndalama zopereka oyimira pa chisankho

Malichi 2025       :               Kuyendera kaundula wa kalembera wapadera

Epulo-Juni 25     :               Oyima pa mpando wa pulezidenti kukatenga makalata awo

Meyi 5 -09, 25    :               Oyimira pa wukhansala kupereka  makalata oyimira pa chisankho 

Juni 11-13, 25 :                Oyimira pa mpando wa pulezidenti ndi uphungu kupereka makalata awo

Juni 18 & 27      :               Kutsindikiza maina a oyimira pa upulezidenti komanso uphungu

Julayi 15                  :           Kutsegulira kwa misonkhano yokopa anthu

Ogasiti 2025      :               Kudinda kwa mapepala ovotera (ballot papers)

Seputembala 5-9, 2025  :    Kufika kwa mapepala ovotera

Seputembala 14, 2025    :    Kutsekera kwa nthawi ya misokhano yokopa anthu

Seputembala 16   :               Tsiku lovota

Seputembala 17- 24         :    Kutsimikizira ndi kuwulutsa zotsatira za pulezidenti           

Seputembala 17-30         :      Kutsimikizira  ndi kuwulutsa zotsatira za aphungu       

Seputembala 17-Oct 7    :      Kutsimikizira ndi kuwulutsa zotsatira za makhansala         

Okutobala 2025    :               Kupereka zipangizo zonse zofunikira ku Nyumba ya Malamulo

Mchingerezi ndondomeko za ntchito zoyendetsera zisankho ziudzazi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *