Ndemanga yathu: Ndondomeko ya Ana Ndi Zimbudzi ya Kongilesi nkutukwana a Malawi

Pitani, kaberekani, MCP ilipira. Izi si Malembo Oyera ayi, koma ndilo lonjezo latsopano kwambiri m’ndondomeko ya MCP ya kampeni yakuti a Malawi awavotele pa 16 Sepetember pano. A President Lazarus Chakwera abwera kachiwiri ndipo tsopano akuti azizagawa K500,000 pa mwana aliyense amene adzabereke pa nthawi yachiwiri ya ulamuliro wake—popeza palibe chinthu chimene akuona chingapindulitse a Malawi pankhani za chuma..

Kabelekaneni tilipira – Chakwera (Image: Nationonline)

Ndipo polembapo mmisamba za michezo kutsimikiza maganizo a chipani cha MCP, Bambo Humphrey Mdyeseni, wotsogolera bungwe la NEEF komanso amene watchuka ndi kugawa ndalama ngati mawa kulibe, akuti ndondomeko ya “bonasi kwa abeleki” ikuyembekezeka kubereka ana 600,000 pachaka boma lizizawononga K300 biliyoni pachaka pa ana okha.

Ndalamazo? Zang’ono basi, akuti Mdyeseni, amene bungwe lawo la NEEF anawononga K8.4 biliyoni ya misonkho yathu kwa ma Shehe, aneneli onyenga ndi azibusa opanda ntchito, akuti zimenezo ndi ndalama zochepa.  

Koma palibe amene wafotokoza ngati mapasa alandila ndalama zawo ziwiri kapena ngati ndi “kupeza mmwana mmodzi, wina waulele”.

Chinaso, chipanichi chikuti ndalamayi izikhala kuthumba mpaka mwana azafike zaka 18. Ndiye kuti ana obadwa nthawi ya a Chakwera atapambana pano, makolo ake azamupatsa mwanayu mchaka cha 2043.

Pomwe ophunzira 10,000 m’mayunivesite akuvutika ndi maphunziro, MCP ili busy ndi ndondomeko ya kubereka. Inde, zikuoneka kuti kugonana kuakhala mfundo ya chuma pa ulamuliro wa chipanichi.

Nkhani ngati izi zimatsimikiza kuti chipanichi kulibe upangili woyendetsa dziko mmene zawonekela mzaka zisanu akhala akulamula. Mbwelera zosathandiza sizingakhale manifesto yakuti anthu akavotele chipani.

Kodi simukukumbuka kuti Chakwera analumbirira kuchepetsa mphamvu za Pulezidenti? Tsopano akugwira mphamvu ngati mwana wagwira botolo la mkaka.

Kumbukirani lonjezo la  ntchito 1 million mchaka choyamba linasanduka fumbi. Tsopano akuti adzapanga 2.3 milion m’dziko limene ma business akugwa kusowa kwa ndalama zakunja, anthu malipilo ochepa komanso chuma kusokonekela.

Kuchoka kwa ana, akuti azamanga zimbudzi za madzi mmasukulu onse.

MCP ikufuna zimbudzi za madzi m’sukulu zonse. Inde, ngakhale kumene kulibe makalasi komwe ana akuphunzira pansi pa mtengo kapena zisakasa, MCP ikufuna azikagwiritsa ntchito zimbuzi za madzi pafupi.

Malipoti amati mwana masukulu 10 aliwonse, atatu alibe zipangizo zokwanila koma chipani cha Malawi Congress chikuyika patsogolo zimbudzi.  Mwina ndichifukwa chakuti amene akudya misonkho yathu nthawi zonse amakhala ku zimbuzi akakhuta, ndiye ntchito zawo zayamba kufanana ndi moyo wawo.

Mu ndondomekoyi nkhani ya feteleza wotsika, Mombera university, nseu wa nyika ndi nseu wa chingale ayiwalamo. Izizi adalonjeza 2020 zidawalaka.Mmalo mwake alonjeza ina yatsopano ku Euthini ndinso mmizinda yonse.

Ngakhale anthu omwe anali ku Bingu stadium anaona kuti ndi zopanda phindu ndipo anatuluka nsanga mu stadium kusiya bamboo Chimwendo Banda akubangula ku ma stand opanda wanthu. Nthano zosalowa mmutu anthu atopa nazo.

A Malawi akufuna Mfundo zosintha umoyo, kufotokoza zonveka kuti mavuto muwathesa bwanji, osati kuzigugudila pa mtima komanso kulonjeza zinthu zopanda pake zosanveka ngati anthu abeleke ndikumanga zimbuzi.

Mkonzi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *