Mkulu wa bungwe losunga zakudya mdziko la National Food Reserve Agency muno a Brenda Kayongo awayimitsa kaye pa udindo wawo.
Wa pambando wa komiti yoyendetsa bungweli a Dennis Kalekeni ati mayi Kayongo adawayimitsa malinga ndi nkhani yakusowa kwa ma lole 13 a chimanga mchaka cha 2022.
A Kalekeni ati komiti yawo yapeza kuti akulu akulu ena a bungweli sanagwire ntchito yawo bwino nchifukwa chimanga chidasowa.
Ma lole 13 a Smollet Kachere omwe ndi mmodzi mwa akuluakulu a chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) adasowa ngati mmene galeta la Eliya mu bayibulo linasowela ndipo mpaka pano a Kachere safotokoza kuti adanka kuti.
A Kachere atasowetsa ma lole adauza bungweli liwalipile K112 million kuwonjezelapo zomwe zinali zodabwitsa ntundu wonse.
A Kachere polankhula ku nyumba ya malamulo pomwe anayitanidwa kuti afotokoze za nkhaniyi, adaulula kuti bungwe la Admaki lakhala likunamiza a Malawi kuti lili ndi matani 38,000 pomwe chimangacho chidabedwa.
“Kulibeko ma tani amakambidwawo, afunseni akulozeleni,” a Kachere adauza a tolankhani
Mpaka pano palibe anayankhapo zomwe ananena a Kachere.
Mtengo wa chimanga pano wakwela kowospya mwakuti mmadela ena monga mboma la Nsanje chimanga chili pa K35,000 thumba la ma kilogalamu fifite.