..fodya chaka chino wochepa kale ndi 60 million kgs
…25% yotenga boma idzutsa mapiri pa chigwa
..nzeru zopezela ndalama zatha ku boma
Munthu yekha yemwe amaganizila kuphazi osati ubongo ndiye angaganize zolanga alimi afodya powatengela ndalama zawo mpaka 25 pelesenti, atelo alimi okwiya mboma la Kasungu atadzidzimuka ndi mfundo ya bungwe la za fodya la Tobacco Commission kuti lizidula 25% pa ndalama za fodya yense wadutsa mulingo.
Mmodzi wa alimi ku Kasungu omwe akhuzika ndi kusinthaku, ati boma la President Lazarus Chakwera liganize mozama nkhanza zomwe likufuna kuwonjezela kwa alimi pakuti ambiri chaka chino sanapeze phindu ndikukwera kwa zipangizo za ulimi.
“Akuganiza ngati amaganizila ku mapazi ndithu, nanga okha adalengeza kuti ogula fodya akufuna 210 million kilogrammes ndipo fodya sanalimidwe wambiri kufika apo, koma akuti yemwe apezeke ndi fodya wambiri amubela ndalama zake. Ndi zosanveka,” watelo mmlimi wina.
Bungwe la Tobacco Commission mu mmwezi wa April lidati ngakhale ogula fodya amafuna ma kilogramme opitilila 200 million, koma alimi adakwanitsa kulima 140 million kilogrammes.
Mukalata yomwe adalemba mkulu wa bungwe la TC a Evans Chilumpha pa 10 June iwo adati alimi omwe alima fodya wambiri ayenela kudulidwa ndalama zawo malinga ndi malamulo oyendetsela mbewuyi.




“Ngati wolima atulutsa fodya wambiri chifukwa cha kalimidwe or chilengedwe, bungwe la TC lizawonjezela mulingo wa fodya kwa olimayo, koma akagulitsidwa fodya lizatenga 25% ya ndalamazo ndipo zotsala zizapelekedwa kwa mulimi,” a Chilumpha adatelo kuti gawo 39 ndime yoyamba ya malamulo a fodya imatelo.
Nkhala kale pa ulimi wa fodya omwe anawuza The Investigator Magazine kuti ndi a Banda aku Lilongwe anati lamuloli palibe boma linagwiritsapo ntchito chifukwa kulima fodya nkowawa.
“Panopa feteleza anadula kwambiri, pa hekitala timalowetsa ma bag 15 feteleza, S compound pa nursery, 8 a D Compound ndinso 5 a CAN. Nthawi zambiri mlimi amapeza 15 to 17 bags pa hekitala, koma apapa kutsata malangizo abwino, mbeu za bwino ena akufika 20 pa hekitala koma boma la Chakwera lati tigawane, malodza ndithu,” atero a Banda.

Mmodzi wa alangizi a mbeu ya fodya lati lamuloli ndi logwetsa mphwayi alimi kuti alimbikile chifukwa ngati boma lakhala likulimbikitsa mbeu komanso ulimi wamakono kuti alimi azikolola zochuluka.
“Apapa ndi pamene tingati alimi omvera malangizo ayamba kupindula, koma hoo boma likuganiza zowapangitsa kuti aleke kulima fodya chifukwa aziwadula zambiri. Ambiri sadapeze phindu, ena kulowetsa K4 million akutulutsa K3 million chifukwa madela ena mvula idapenga,” adatelo mlangiziyu ku msika wa Lilongwe.
Mzaka zisanu pansi pa ulamuliro wa chipani cha Malawi Congress (MCP) motsogozedwa ndi President Lazarus Chakwera a Malawi omwe amapeza ndalama za kunja akhaula ndi Mfundo za tsopano zomwe bomali lakhala likuyika.
Poyamba bomali lidayika lamulo kuti aliyense wosunga ndalama za kunja mma bank- ndalama zake azizisintha mpaka 60%, zomwe zidapangitsa kuti ambiri atseke ma akaunti awo komanso mabungwe akunja aleke kutumiza ndalama koma kumagulilathu katundu.
Pakadali pano bungwe la za chuma padziko lonse la IMF lidaleka kuthandiza dziko la Malawi chifukwa chakuti boma lidaphela kuyendetsa chuma chake bwino komanso katangale. Ngati a Malawi angasankhe boma la MCP ndiye kuti chuma cha dziko la Malawi chizagwerathu chifukwa palibe angalithandize.
Pakadali pano tikufufuza anthu ogwira mma bank, Auction Floors ndi ena omwe akusintha ndalama za fodya powakakamiza alimi kuti atsegule ma account andalama za kunja, anthuwo nkumasintha ndalamazo pa mitengo za mmisika ina (black market)
NDEMANGA YA MKOZI WATHU
Nzeru zikatha, amatha kuzisiya: Ntchito ya ukhansala, kaya u MP kaya u President umene ndi ntchito zongozipeleka osati zokakamizana ngati bambo kaya mayi kulera mwana yemwe abeleka okha.
Chodabwitsa nchakuti andale aku Malawi amakakamila pa udindo ngakhale zinthu zikuwalaka. Nthawi zambiri amaganiza zolanga anthu osauka kale komanso omwe alibe mphanvu.
Boma ngati nzeru zatha zoti angapezele ndalama za kunja, atha kuzisiya ndikulola a Malawi ayesele ena mwina zinthu kusintha. Kuyambila 2023 pomwe adagwetsa ndalama ya kwacha, unmphawi wafika pena, ndalama idatha mphanvu zinthu zidakwela kwambiri.
Palibe Mfundo zomwe boma la Kamba olo nthawi kuti mavutowa ayamba kuchepa kapena kutha liti, chomwe tikunva ndi nkhanza amwamba pa nkhanza. Funso nkumati kodi nzeru za bomali ndi kulanga anthu basi.
Pompano boma lidavomeleza a Green Belt kugula galimoti la K450 million ngakhale kampani yake ya Salima Sugar ikufuna ndalama zoti a Malawi ayipatse ikonzele zinthu. Ulemelero wawo ndiye akuyikapo mtima, koma mavuto a Malawi alibe nawo ntchito.
Kulanga mulimi poti watulutsa fodya wambiri atatsatila Mfundo za ulimi singakhale njira yakuti boma lipezele ndalama za kunja. Kulima nkowawa, ndipo kumalowa zambiri.
Monga wanenela wina, bomali silikuganiza ngati munthu wakuti ali ndi ubongo koma kuphazi. Ngati zikuwalaka, atha kuzisiya pa Seputembala 16, anzawo ayeseko mwina a Malawi mkupuma!