Chakwera adabwitsa anthu pa za katangale

President Lazarus Chakwera wadabwitsa a Malawi pomwe anati iye akulimbana ndi katangale zomwe anthu ena sakukondwa nazo. Anthu ambiri pa tsamba la mchezo adabwa naye mtsogoleri wa dziko linoyi ngati amatha kunena zoona poti katangale wafika ponyansa kwambiri mu ulamuliro wake.

A Chakwera akuti athana ndi katangale

Pansi pa abusa a Chakwera katangale wakula kwambiri ndipo chuma komanso ma pulogalamu aboma asokonekela kuposa zaka za mmbuyomu, zomwe zili zosiyana ndi ma president asanu omwe adalamulilapo dzikoli. A Malawi ambiri pano ndi osauka, alibe chakudya komanso zinthu zikukwela chifuna nduna ndi akuluakulu osankhidwa ndi a Chakwera akusakaza chuma chaboma molapitsa.

Abusa a Chakwera pansi pa iwo, mkulu wa bungwe lothana ndi katangale la ACB wakale Mai Martha Chizuma adamangidwapo pomwe anthu omwe awazungulira abusawa ankafuna kuthana nawo pakuti amalimbana ndi katangale.

President Chakwera mmalo mosafuna kunva chilungamo anayika komiti ya bodza yomwe inafufuza zosiyana komanso panafika pofuna kuchotsa Mai Chizuma.

Anthu aku banja la Chakwera nawo alemela modabwitsa mpaka kukumba miyala ya mtengo wapatali ndipo Mlembi wa mu office mwawo Mai Colleen Zamba, nduna ya za miseu a Jacob Hara komanso Mlembi wa ku unduna wa za magesti a Alfonso Chikuni anatchulidwa mu katangale wofuna kupanga za chinyengo popanga makampani awo nkumanamizila kuti ndi a Shehe wina wotchuka waku Dubai.

President Chakwera naye amadya nawo mu za chinyengozi, mwakuti mpaka pano palibe adayimisidwa ntchito.

Pansi pa a Chakwera nduna zina monga a Chimwendo Banda anatchulidwa kuti amakatapa ndalama kwa nzika za mdziko la Burundi koma palibe chomwe Abusa a Chakwera adachita.

Chimwendo Banda anatchulidwa kuti amakatapa ndalama kwa nzika za mdziko la Burundi

Feteleza naye adasokonekela ndi katangale pomwe nduna za boma la Abusawa zinakasaka ku malo ogulitsila nyama, ena malo ogulitsila mankhwala monga nduna ya za ulimi a Sam Kawale adatengana ndi anzawo kuti apeleke feteleza wa  ndalama zambiri zodutsa K700 billion. A Kawale adapita pa mawayilesi kukanena kuti makampani wo adali akunja, kunamiza a Malawi. Koma palibe chinachitika.

Anthu omwe anakhuzidwa ndi kosokonekela kwa K300 billion zomwe anapatsidwa a Zuneth Sattar anabwelelenso ku ntchito zawo ena mu office mwa abusa a Chakwera.

“Katangale akulimbana naye mwina ku uzimu, pamaso aliyense akudziwa iwo ndiye mkulu wa katangale, amakonda katangale, amayikila ku mbuyo akatangale ndipo sangachotse ntchito anthu akatangale kuopa kuwululidwa. Nthawi zina akanamadya ndalama za katangale osatenga a Malawi ngati ogunata,” wakalipa wina pa tsamba la mchezo la newspaper ina.

Ku nkhani ya kusowa kwa ndalama za kunja a Chakwera adauza nyumba ya malamulo kuti Amwenye ndiye akusowetsa ndalamazi koma pali umboni okwanila ku ena ogwira ku Nyumba ya Chakwera, mmodzi mwa akuluakulu a Police a Ackis Muwanga onse akugulitsa ndalama za kunja mosatsata malamulo ndipo palibe chomwe Presidentiyu achitepo olo atapatsidwa umboni.

Atangolowa pa udindo, a Presidentiwa ndi anyamata awo anasowetsa ma truck 13 a chimanga cha boma ndipo membala wamkulu wa chipanichi a Kachere adauza nyumba ya malamulo kuti chimangachi amagawana akulu akulu a boma ndi MCP koma palibe adamangidwa.

Kenaka phwando la akakowali lidafika ku thumba lothandizila matenda a Covid pomwe a Chakwera adachotsa a Ken Kandodo omwe samafuna powopa kuti ndi mbale wa Kamuzu Banda. Koma ena onse adaba za Covid palibe chomwe abusawa anachita.

Ku nkhani za mafuta nako kuli ndeu pakati pa Mai Zamba ndi ena kukanganilana mgodi wa mafuta omwe akugula mokwela kuti azichotsapo cha khumi, koma ngakhale zonse zakhala zikukambidwa a Chakwera akuti akulimbana ndi katangale.   

Pakadali pano bungwe la ACB lilibe mtsogoleri poti a President Chakwera akufuna a Hilary Chilomba a chipani chawo kuti akhalepo kuti azimanga otsutsa boma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *