Anthu omwe akupikisana mmadela omwe muli zinduna kapena aphungu kale a chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) adandaula kuti masankho osankha oti azayimile pa zisankho za aphungu aku nyumba ya malamulo zikuchitika mwa chinyengo.

Mmadela okwana 15 pakadali pano zisasnkho zasintha mwadzidzi mopanda chifukwa ndipo anthu ambiri akuti izizi akuchita dala akulikulu la chipani pofuna kuti nduna zidutse moyela komanso aphungu ena.
“Ku Kasungu South apanga la Mulungu pa six zifukwa zosanveka cholinga anthu alephele kumema ma supporters. Akukondela a nduna a za chuma a Simplex Chithyola Banda. Ku Dowa kwa a nduna a Sam Kawale anthu angowuzidwa loweluka kuti masankho pa chitatu (9 April) mmalo mwa pa 18,” atero anthu ofuna kupikisana.
Madela ambiri nduna zambiri anthu sakuzifuna mwakuti kafukufuka The Investigator Magazine wa ndale adawonetsa kuti nduna zonse za kuchigawo cha ku mpoto zomwe ndi a Uchizi Mkandawire, a Ken Zikhale Ng’oma, a Jakobo Hara ndi a Noah Chimpeni sangapambane pa mipando ya phungu mmadela mwawo.
Spikala wa Nyumba za malamulo ndinso nduna ya za malonda a vitumbiko Mumba nawo mwayi wawo ngochepa.

Mchigawo cha pakati, nduna ya za ma boma ang’ono a Richard Chimwendo Banda ndinso a Peter Dimba aku unduna wa za ntchito ndi okhawo akuwonetsa nyonga zakuti atha kupambana mpando wa phungu. Nduna zina zonse ndi aphungu ambiri azagwa olo atayimila chipani cha Kongilesi.
Ku chakummwera palibe nduna ipambane. Ndipo maboma ambiri ku mmwera, ma boma ngati Ntcheu, Mchinji, Nkhotakota ndi Kasungu a Kongilesi ipeza aphungu otsikilapo kuposa mchaka cha 2019. Ku Mpoto boma la Mzimba lokha madela awiri akuoneka atha kuvotela phungu wa MCP.
Pa u President, President Lazarus Chakwera ayenela kukwanilitsa zina mwa malonjezano ake akulu akulu mamsiku pafupifupi 160 atsalawa kuti anthu mwina angakamuvotele ngakhale pa chigawo chapakati. Mwa anthu 100 aliwonse kafukufuku wa ndale akuonetsa kuti a Malawi odutsa 80 akuti a Chakwera alephela pa udindowu.