Zadziwika kuti kampani yoyenga mafuta ya Addax Petroleum ndiyo inatumiza mkulu wa bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) a Henry Kachaje kupita ku Dubai kuti akachite zokambirana ndi mtsogoleri wa dziko la Malawi, Dr Lazarus Chakwera kuti asinthe ganizo lake loyamba kutsatira mgwirizano wogulitsana mafuta pakati pa maiko (G2G) ndi kusiya kugula mafuta kuchokera ku makampani ogulitsa mafutawo, monga idafotokozera The Investigator Magazine.
A Kachaje pamodzi ndi wamkulu wa national Oil Company a Clement Kanyama, anathandizidwa ndi mlembi wamkulu ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna a Colleen Zamba komanso nduna imodzi ya boma (yemwe dzina lake silinatchulidwe) popanga upo wosokoneza kayendetsedwe ka mafuta omwe anali atafika pa doko la Tanga mdziko la Tanzania pa 27 Disembala chaka cha 2024. Iwo adachita izi pofuna kukwaniritsa kuti mgwirizano wogulitsana mafuta pakati pa maiko sungapindule.
Pamene a Kanyama ndi a Kachanje anakaonekera ku Komiti yoona za mafuta ndi magetsi ku Nyumba ya Malamulo lachisanu, iwo anafotokozera dala molakwitsa kuti analibe magalimoto oyenerera omwe angabweretse mafuta ku Malawi. Pachilungamo pake, NOCMA inkachedwetsa dala pofuna kukolezera vuto, pofuna kunyozetsa ndondomeko yogulira mafuta yomwe inakhazikitsidwa posachedwapa imene imapangitsa mtengo wa mafuta kukhala wotsika ndi $89 pa tani (K300,000) kusiyana ndi makampani omwe ankapereka kale omwe akungosunga mafutawa.
Lachisanu kummawa, a Kachaje ananamiza komiti yaku Nyumba ya Malamulo kuti NOCMA inalibe njira zotumizira mafuta omwe inagula pakatikati pa mwezi wa Disembala. Potengera ochita malonda a zamtengatenga a mdziko lino, akuti iyi inangokhala njira yofuna kugwiritsa ntchito ochita malonda a za mtengatenga akunja zomwe zingapangitse dziko lino kutaya ndalama pafupifupi K30 biliyoni kwacha (US$ 9.7 miliyoni), mmalo mogwiritsa ntchito ochita malonda a za mtengatenga a mdziko lino omwe akhoza kungolipidwanso ndalama ya kwathu konkuno yokwana K17 biliyoni kwacha.
A Kachaje ananamanso kuti ochita malonda a za mtengatenga a mdziko muno alibe kuthekera.
Zikuonetsa kuti Mtsogoleri wa dziko lino akulephera kuthana ndi katangale yemwe wamanga nthenje pa kagulidwe ka mafuta kaamba ka mphekesera zakuti ena mwa akubanja kwake agwidwa pakhosi ndi makampani ogulitsa mafuta.
OGULITSA MAFUTA OMWE ANAPEREKA “CHAKHUMI” AKUFUNA MGWIRIZANO WOGULITSANA MAFUTA PAKATI PA MAIKO UTHETSEDWE
Vuto la kusowa kwa mafuta lafika povuta kwambiri makamaka kaamba ka katangale osati kusowa kwa ndalama zakunja. Ndondomeko za ku NOCMA zadzazidwa ndi njira zogulira mafuta za katangale monga kugulitsana pachiweniweni, ziphuphu ndi kupereka komishoni zomwe zimafika US$100,000 pa mwezi zomwe zimaperekedwa kwa andale komanso akuluakulu a boma ku nthambi zosiyanasiyana kuphatikizapo ku Nyumba ya Boma, Ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna, NOCMA, Unduna wa za magetsi ndi mphamvu komanso posachedwapa ku MERA.
Pali magulu atatu amene akulimbirana ntchito yoyitanitsa mafuta: gulu lomwe langosankhidwa kumene ndi mtsogoleri wa dziko lino, momwe muli alangizi, anthu ochokera ku maunduna komanso akatswiri; gulu lomwe lilipo pano logula mafuta limene limatsogoleredwa ndi Mlembi wamkulu ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna a Zamba, yemwenso ndi mkulu wa NOCMA; komanso kagulu ka a ndale omwe ali ndi maubale apadera ndi a kubanja la a Pulezidenti.
Kuti afike pa mgwirizano, wokhala ndi magulu atatu opereka mafuta kuchoka pa magulu asanu ndi limodzi zidachokera ku gulu la ku Sbanja la Pulezidenti, pomwe operekera mafuta otsalawo akuchokera ku gulu la NOCMA komanso la Mlembi wamkulu wa ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna. Dongosolo limeneli lidapangitsa kuti opereka mafuta omwe anasankhidwa ndi gulu la NOCMA komanso la Mlembi wamkulu wa ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna akonderedwe kusiyana ndi ena. Mwatsoka, gulu la kubanja kwa a Pulezidenti, lomwe lili ndi ndondomeko yayikulu ya kapezedwe ka mafuta, lidasokoneza ndondomeko yobweretsera mafuta kaamba ka nkhani za malipiro.
Mu mwezi wa Sepitembala, yemwe anali gavanala wa bank yayikulu ku Malawi, Dr Wilson Banda adapereka nkhawa zake kwa Pulezidenti zokhudza ndalama zoposa US$15 miliyoni zomwe zidaperekedwa ku NOCMA kuti alipire omwe amatibweretsera mafuta, koma panalibe ngakhale mmodzi yemwe analipidwa. Potengera omwe atitsina khutu, izi zinathandizira kuti Dr Banda achotsedwe pa udindo ngati mkulu wa bankiyi pakuti adasonyeza kulimbana ndi magulu a mphamvu omwe amamulamulira Pulezidenti Chakwera.
Gulu latsopano lomwe muli a Pastor Zach Kawalala ndi Hellen Buluma ngati alangizi pamodzi ndi mayi Monica Chakwera ngakhale zili zosatsimikizika akuona kuti ndondomeko yogula mafuta pakati pa maiko ndiyabwino kusiyana ndi kugula kuchokera kwa amkhalapakati.
Njira yogula mafuta pakati pa maiko ikukanidwa ndi gulu la NOCMA komanso la Mlembi wamkulu wa ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna.
Gulu lochokera ku Unduna, lomwe likutsogoleredwa ndi Nduna ya za Magetsi ndi Mphamvu a Ibrahim Matola akufuna ndondomeko yogulitsana mafuta pakati pa maiko ndipo adakonza dongosolo kuti Pulezidenti apite ku Dubai kuti akachite zokambirana ndi atsogoleri kuti athe kumatigulitsa mafuta.

Dongosololi likuoneka kuti likhoza kuchepetsa mtengo wobweretsera mafutawa; komabe, dziko la Kenya likuganiza zosiya kutsata ndondomekoyi kaamba kakuti siyikupereka phindu lomwe linkayembekezereka.
Nyuzipepala ya The Investigator Magazine inafotokoza kuti ganizoli lisadaperekedwe, Mlembi wamkulu ku Unduna wa za magetsi ndi Mphamvu a Alfonso Chikuni ndi a Kanyama omwe amagwira ku NOCMA, adapita kaye ku Kenya kukaunika njirayi. Atalephera kupeza phindu, adadzudzula ndondomekoyi mu lipoti lawo lomwe titalitambasule mu nkhani yathu yotsatira.

A gulu la Mlembi wamkulu wa ku ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna a Zamba, Chikuni, Kanyama ndi Kachaje ali mgulu logula mafuta lomwe lidakhazikitsidwa ndi Pulezidenti. Ngakhale zili chonchi, akuoneka kuti sakukhutitsidwa ndi dongosololi, zomwe zikuonetsa kuti NOCMA siikukhudzidwanso mu ndondomeko yatsopanoyi kuchokera pamene linalengezedwa.
Ofalitsa nkhani anapatsidwa ndalama kuti apitirize kunyozetsa ndondomekoyi pomwe gululi lidapitiriza kugawa mafuta, pomwe ena anamenyetsa nkhwangwa pamwala kuti ndondomekoyi ilephereke. Gululi lawonjezeranso nkhani za njira zobweretsera mafuta mu ndondomeko yolandira ziphuphu.
Ulendo wa ku Dubai, Kachaje atengera gulu la Addax kwa Chakwera
Mkulu wa Bungwe la MERA, yemwe sanali nawo pa gulu lopita ku Dubai, anapita ku Abu Dhabi pofuna kukapangitsa nkumano pakati pa gulu la Addax ndi Chakwera. Koma ndizokaikitsanso ngati nkumanowo udachitika.

Kampani ya Addax idalipirira mkulu wa MERA-yu mafuta komanso malo ogona pa ulendo wa ku Dubai, komwe mkuluyu sadakakhale nawo pa zochitika zilizonse za a Pulezidenti. M’malo mwake, mkulu wa MERA-yu adapita kukakometsa kampani ya Addax ndi kampani ina yoperekera mafuta.
Potengera yemwe watitsina khutu ku MERA, a Henry Kachaje ndi a Clement Kanyama ali ndi chidwi chapadera ndi ndondomeko yatsopano yobweretsera mafuta pogwiritsa ntchito makampani awiri. Izi zili chonchi kaamba kakuti amapindula ndi ndondomekoyi. Yemwe watitsina khutuyu anafotokozanso kuti bungwe la MERA silinalipireko kalikonse pa ulendowo.
Pulezidenti atangolengeza za kusintha kwa ndondomeko yogulira mafuta kuti izitsatira mgwirizano wa pakati pa amaiko, kampani yogulitsa mafuta ya Addax inaitanidwa kuti ibwere ku Malawi ndi kudzakumana ndi Pulezidenti komanso akuluakulu ena kuti akakamize kuti ndondomeko yomwe ilipo isasinthidwe. Ngakhale anayesera kangapo, nkumano ndi Pulezidenti siunatheke. Zotsatira zake, Pulezidenti anapita ku Abu Dhabi kukakambirana zogula mafuta kuchokera kwa oyenga mafuta aku UAE, potengera ndi omwe atitsina khutu ku Ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna. Otitsina khutu anaululanso kuti, ngakhale a Kanyama ndi a Kachaje anakhudzidwa kwambiri, koma omwe ankawatuma ankazindikirika mosavuta.
Nyuzipepala ya The Investigator Magazine ikhoza kuulula, potengera zomwe yapeza kuchokera kwa anthu odalirika, kuti Pulezidenti adapatsidwa kuti aunike mgwirizano womwe kampani ya Addax izidzagula mafuta ku kampani ya ARMCO ya mdziko la Saudi Arabia.
Potengera zomwe akuluakulu aboma ananena, ganizo loyamba logula mafuta ku kampani ya ARMCO lidasokonezeka pa nthawi imene thumba la Badea Fund lidapereka ngongole yogulira mafuta yokwana $50 miliyoni. NOCMA inapatsidwa fomu kuti lipemphe kugulitsidwa mafuta popanda amkhalapakati koma siinachitepo kanthu ,pakuti akalandira mafuta popanda ankhalapakati kuchepetsa ziphuphu zimene amalandira.
Mafuta ogulitsana pakati pa maiko ndi otsika mtengo kusiyana ndi omwe amatibweretsera panowa.
Zomwe zalembedwa mu The Investigator Magazine zikusonyeza kuti kampani ya Hass ikugulitsa diesel pa mtengo wa US$273 pa tani ndipo petrol akugulitsidwa pa mtengo wa US$255 pa tani. Tikasiyanitsa, Kampani ya Addax ikugulitsa diesel pa mtengo wa US$215 komanso petrol pa mtengo wa US$ 225.
Mafuta apangozi omwe anagulidwa kudzera mu ndondomeko yogula mafuta pakati pa maiko adafika pa mtengo wotsikirapo wa US$184 zomwe zidapangitsa kupulumutsa US$89 pa tani ya diesel komanso US$194 ya petulo, zomwe zinapangitsa dziko kupulumutsa US$61 pa tani. Kusiyana ndi omwe akutigulitsa mafuta kudzera ku NOCMA. Izi zikusonyeza kuti Amalawi akhala akuphinjika kwa nthawi yayitali.
“Kuthekera kogula ku Dubai kapena ku Abu Dhabi motsika mtengo mopanda ankhalapakati kungathandize kukhala ndi mitengo ya mafuta yokhazikika komanso yotsika. Nzokhumudwitsa kuti magulu ena akutsutsana ndi njira imeneyi,” anatero wina yemwe anatitsina khutu ponena kuti omwe akutsutsana ndi njira yatsopanoyi akupindula ndi katangale pa mitengo yowonjezera yomwe imaikidwa pamwamba pa mitengo yomwe owagulitsa mafuta amaika.
Mafuta asiidwa ku Tanga kwa masiku 11, NOCMA ilephera kupeza njira zobweretsera mafutawo
Mafuta ochuluka malita 50 miliyoni omwe anapezedwa kudzera mu njira yazadzidzidzi, anafika pa doko la Tanga pa 27 Disembala 2024. Nduna ya za Magetsi ndi Mphamvu a Ibrahim Matola adakondwera ndi kulengeza ku dziko lomwe latopa ndi kudikira pa mizere ya mafuta kuti vutolo tsopano latha, potengera ndi mphamvu zatsopano zomwe anapatsidwa ndi Pulezidenti. Akuluakulu aku Unduna wa za Magetsi ndi Mphamvu, OPC, NOCMA,ndi MERA anali ndi zolinga zina. Adachedwetsa kutumiza magalimoto okatenga mafutawa kwa masiku 11. Pamene kafukufuku anakula, NOCMA inalengeza lachinayi, pa 9 Janyuwale- tsiku lomwe Matola amayembekeza kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino.
Maguluwa anabalalitsa a Matola, Pulezidenti komanso Amalawi onse, pozindikiranso kuti palibe chomwe chingachitike. Kusachitapo kanthu kwa Pulezident kukusonyeza kufooka kwake, kulola kuti magulu otsutsana naye pogula mafuta azikhala ngati atsogoleri a dziko. Pulezidenti Chakwera wangokhala chidude.
Magulu osokonezawa safuna kusiya kulamulira kayendetsedwe ka mafuta kufika mdziko muno, cholinga chofuna kupereka mpanipani komanso kudalira kwambiri magalimoto awo aku Tanzania omwe amapangitsa dziko kupereka ndalama zoposa US$9.8 Miliyoni tikasiyanitsa ndi magalimoto a kwathu konkuno.

Potsatira mitengo yatsopano yotengera katundu kuchokera ku doko la Tanga kufika ku Lilongwe, magalimoto a ku Malawi azilipidwa m’makwacha, kupangitsa kuti ndalama zakunja zisamagwiritsidwe ntchito. Azilandira K349.93 pa lita pa malita okwana 50,850,000 zomwe zikukwana K17,793,940. Magalimoto a kunja malipiro awo ndi US$9,885,522 pogwiritsa ntchito ndalama zakunja. Ndalama zonsezi ndizokwanira kugula mafuta owonjezera a magalimoto okwana 300 omwe angatidutsitse mwezi wa February. Nkhalakale pa malonda a za mtengatenga anati a Pulezident akuyenera kulowererapo pakuti nkhanizi ndizofunikira kwambiri.
Palinso nkhawa zina kuti anthu ochokera ku NOCMA komanso MERA akumawafikira anthu kumawauza kuti asakatenge mafuta ku Tanga, powalonjeza migwirizano. Mchitidwe Wadala wonyozerawu unatsimikizidwa ndi anthu awiri ochita malonda a zamtengatenga ku Lilongwe.
A Kachaje ananena kuti ochita malonda a za mtengatenga a ku Malawi kuno alibe kuthekera zomwe zinatsutsidwa kwa ntuwagalu ndi bungwe loona za mtengatenga mziko lino.
Mu nkhani yathu yotsatira tidzakamba za akuluakulu okhudzidwa mu bizinesi ya mafuta, makampani omwe akukhudzidwa, zitsanzo za ziphuphu komanso njira zomwe amagwiritsa ntchito pofuna kulamulira nkhani ya kapezedwe ka mafuta m’Malawi muno.