Zisatikhuze MEC ikanila a Police nkhani ya Mithi

Bungwe la za chisankho mdziko la Malawi (Malawi Electoral Commission) lawuza bwalo la milandu ku Lilongwe kuti silinakadandaule kuli konse pa zomwe mkulu wodziwika pa masamba a mchezo a Facebook a Julius Mithi analemba zokhuza kusowa kwa mayina a anthu omwe adalembetsa kuti azavote pa 16 September chaka chino.

A Mithi kutuluka mu khothi

Malinga ndi zikatala zomwe a The Investigator Magazine awona ku Court la Magistrate mboma la Lilongwe, bungwe la MEC lazitsatsa kuti ilo silinakapeleke dandaulo kwa wina aliyense zomwe zidapangitsa kuti a Police amange a Mithi mwezi wathawu.

The Investigator Magazine idapeza kuti mmodzi mwa akuluakulu a Police a Akis Muwanga, Mlembi wa mkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) a Richard Chimwendo Banda ndinso yemwe akugwirizila udindo wa Mkulu wa bungwe la za katangale a Hilary Chilomba adakumana mwanseri ndikupangana zomanga onse ostutsa boma, ngati njira imodzi yowawopyeza kuti asamadzuzule boma la President Chakwera.

Chikumanilane akuluakuluwa, a Mithi, wachiwiri kwa mtsogoleri wa DPP mchigawo chapakati a Alfred Gangata, anzawo ku chigawo cha ku mwera a Joseph Mwanamvenkha, Phungu wa Aford wa ku Mzimba a Yeremiah Chihana komanso ena akhala akumangidwa milandu yosadziwika mutu wake.

A Mithi omwe anakaonekela ku bwaloli lolemba sabata lino komwe a Police anati mboni zawo zones kuphatikizapo a Sambo a ku National Registration Bureau (NRB) kunalibeko ndipo ambali ya boma anapempha kuti mulandu uyime kaye.

A Mithu atanjatidwa ndi apolisi aku Lilongwe

Mmodzi wa akatswiri azamalamulo, wati nkhani za kaundula wa zisankho amayendetsa ndi bungwe la MEC ndiye pakadali pano zikhala zodabwitsa kuona bungwe lina la NRB likudandandaula ntchito za bungwe lina.

“Mulandu apapa palibe usanayambe,”  watelo mmodzi wa ma loya mdziko muno.

Pakadali pano mulanduwu awuyimitsa pamene boma likusaka mboni komanso wodandaula pa nkhaniyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *