…feteleza mwalandira- Sam Kawale
…Ombudsman akwiya ndi chipwirikiti
Pamene nduna ya zaulimi a Sam Kawale amawuza atolankhani ku Lilongwe kuti ntchito yogawa zipangizo za ulimi yayenda bwino, anthu aku Ulongwe ku Balaka analawilila ku office ya za ulimi kukadandaula akukanika kupeza feteleza.
Alimiwa akuti makuponi awo ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo monga feteleza akumapezeka kuti aguliridwa kale zipangizozi, iwo akapita pa msika kuti akagule
M’modzi wa alimiwa, a Stanley Kapinga ochokera ku dera la Mfumu yaikulu Kalembo, ati izi zachuluka m’malo ogulira fetelezawa mokuti akapita pa msika kuti akagule zipangizozi monga feteleza akumabwezedwa.
Iwo adandaula kuti izi zikhudza ulimi wawo potengera kuti kukhala kovuta kupeza zipangizozi
Mkulu wa zaulimi m’boma la Balaka David Ali watsimikiza kuti iwo akhala akulandira madandaulo oterewa koma kuti zosamwitsa zonse azitumiza ku boma kumene pakadali pano akuyembekeza mayankho.
Ombudsman naye wakwiya ndi chipwilikiti
Amalawi apitirira kukumana ndi vuto lakusowa kwa chakudya ndipo izi ndichifukwa cha a pulezidenti a Lazarus Chakwera komanso nduna yawo ya za ulimi a Sam Kawale omwe alephera kuyendetsa bwino ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo zomwe alimi ambiri sizinawafikire mu nthawi yabwino.
Malingana ndi kafukufuku wathu, mu malo ambiri osungiramo katunduyu mulibemo ndipo makampani omwe anasankhidwa kuyendetsa ntchitoyi ena alephera kugwira ntchito yawo pomwe ena angosunga katunduyu chifukwa chosalipilidwa ndalama zawo.
Ndipo chipwirikitichi sichinasangalatse mkulu woteteza anthu ku zinthu zosiyanasiyana (ombudsman) a Grace Malera omwe mu kalata yokwiya ya pa 20 Disembala 2023 yomwe ife tawona yopita kwa mlembi wamkulu mu Unduna wa za Malimidwe komanso bungwe la SFFRFM lomwe likutsogolera kuyendetsa ndondomekoyi. Pakadali pano, a Malera ati akufuna kuti akuluakulu alowererepo kukonza chipwirikitichi.
A Malera anayenda m’maboma okwana 25 kuchita kafukufuku wa chipwirikiti cha ndondomekoyi.
M’mbuyomu, a pulezidenti a Chakwera ndi nduna ya za ulimi a Kawale ananamiza Amalawi ponena kuti dziko lino lidzakhala ndi fetereza okwanira koma m’mene zinthu ziliri pakadali pano, mkulu woteteza anthuyu (ombudsman) walamula kuti mayankho aperekedwe pachifukwa chomwe fetereza sakupezekera.
“Zadziwikanso kuti fetereza obereketsa wa UREA ndiwochepa m’maboma omwe anayenderedwa. Izi ndizodandaulitsa potengera kuti mmadera ena mvula inayamba kale kugwa. Fetereza akumayenera kuperekedwa msanga kwa alimi ndicholinga choti athiridwe mu nthawi yabwino. Ndi ndondomeko zanji zomwe Unduna wa za Malimidwe wayika pofuna kuthana ndi vutoli,” atero a Malera mchikalata chomwe tawona.
Chinyengo pa ziphatso zaunzika
Alimi ena okwiya awuza ofesi ya Ombudsman kuti ziphatso zawo za unzika zomwe zikugwiritsidwa ntchito powombola zipangizo zotsika mtengozi zinagwiritsidwa kale ntchito ndi anthu ena chonsecho iwo sanapitepo ku shopu iliyonse.
“Zadziwikanso kuti alimi ambiri sanakwanitse kuwombola zipangizo zawo chifukwa sisitimu ikuwonetsa kuti maina awo anatenga kale katundu wawo. Izi zikudabwitsa chifukwa anthuwa sanapitepo ku shopu iliyonse,” akutero a Malera.
Iwo anati mwachitsanzo, pa malo ogulitsira a Mamina ku Ntchisi, madandaulo 70 anaperekedwa, p Chatoloma ku Kasungu, kunali madandaulo 20, ku Mnkhota m’boma lomweli kunali madandaulo asanu. Anthu omwe anapezana ndi vutoli mayina awo anatumizidwa ku maofesi a zaulimi a mmadera awo koma mpaka pano palibe chomwe chachitika.
A ombudsman afunsanso Unduna wa zaulimi ngati ukudziwa kuti bungwe la SFFRFM limakana kulandira ziphatso za unzika zapadera zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri asemphane ndi mwayi wopeza zipangizozi.
Malingana ndi a Malera, iwo atinso nambala yomwe inaperekedwa kuti anthu aziyimbako mwaulere akakumana ndi zovuta pa nkhani ya zipangizozi ndiyopanda pake chifukwa nthawi zina siyimankhidwa. Nkhani ya netiwoki nayonso ndi vuto linanso. Kuwonjezera apo, anthu mmadera en akumayenda mitunda itali itali monga 70 KM kuti apeze zipangizozi monga ku Chitipa.
Kutsatira izi, a Malera anapereka masiku 14 kuyambira pa 20 Disembala, 2023, ku Unduna wa za Malimidwe kuti uwayankhe mafunso awo monga mwa malamulo makamaka gawo 123 ndinso gawo 5 la malamulo a Ombudsman (Ombudsman Act) ndi ena omwe amapereka mphamvu ku ofesi yawo kufufuza madandaulo aliwonse okhudza chinyengo cha mtundu uliwonse cha wogwira ntchito m’boma.
Ena mwa maboma omwe ofesi ya ombudsman inakayendera ndi monga Chiradzulu, Blantyre, Mwanza, Neno, Phalombe, Mulanje, Nsanje, Chikwawa ndi Thyolo, Mangochi, Machinga, Zomba, Balaka, Karonga, Chitipa, Nkhata Bay, Rumphi, Mzimba, Kasungu Ntchisi, Dowa, Ntcheu, Salima, Dedza ndi Mchinji.
Alimi ochuluka, m’mawa wa ladzulo (Lachiwiri pa 2 January) amang’ala pa ofesi ya za ulimi ya Ulongwe EPA m’boma la Balaka, kudandaula kuti makuponi awo ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo monga feteleza akumapezeka kuti aguliridwa kale zipangizozi, iwo akapita pa msika kuti akagule
M’modzi wa alimiwa, a Stanley Kapinga ochokera ku dera la Mfumu yaikulu Kalembo, ati izi zachuluka m’malo ogulira fetelezawa mokuti akapita pa msika kuti akagule zipangizozi monga feteleza akumabwezedwa.
Iwo adandaula kuti izi zikhudza ulimi wawo potengera kuti kukhala kovuta kupeza zipangizozi
Mkulu wa zaulimi m’boma la Balaka David Ali watsimikiza kuti iwo akhala akulandira madandaulo oterewa koma kuti zosamwitsa zonse azitumiza ku boma kumene pakadali pano akuyembekeza mayankho.