Ku Balaka njala yavuta

..anthu akugona ku Admarc

Pamene boma kudzela ku unduna wa za ulimi likuziguguda pa ntima kuti likuthana ndi njala, ku Balaka anthu akugona ku nsika wa Admarc kudikila chimanga chomwe sichikufika

Zizindikiro zoti anthu ambiri akuvutika ndi njala zinawonekera usiku wa lachiwiri pomwe anthu ambiri anakhamukira ndikukagona ku depoti ya Admarc m’boma la Balaka kudikirira kuti agule chimanga pakucha kwa lachitatu.

anthu kugona ku Admarc kudikira chimanga ku Balaka

Patatenga nthawi yayitali depotiyi isakugulitsa chimanga, lachiwiri anthu anamva mphekesera zoti depotiyi iyamba kugulitsa chimangachi lachitatu choncho iwo anathamangira ku msikawu kuti akakhaliretu pa mzere kudikirira nthawi yogula tsiku lobweralo.

Malingana ndi anthu omwe tinacheza nawo, iwo anati anapanga izi ndicholinga chofuna kusapereka mwayi kwa mavenda kukhala oyambirira kugula chimangacho.

Anthuwo anati ogwira ntchito ku malowa amayamba kupereka ziphaso zogulira kuyambira nthawi ya 7:30 ku mamawa.

A Martha Asibu ochokera kwa Sosola m’bomali anati nthawi zambiri mavenda ndiamene amawakhomelera chifukwa ndiamene amaphangira kugula chimangachi polemba anthu a padera oti awakhalire pa mzere.

“Ndinaganiza zodzagona pa mzere pofuna kuti ndidzakhale woyambirira kugula chimangachi. Ndikanapanda kutero sindikanapeza mwayi wogulanso chimangachi chifukwa mavenda ndiamene amaphangira,” iwo anatero.

Koma pofika nthawi ya nkhomaliro (lachitatu) anthuwa nkuti anali asanayambe kugula chimangachi.

Mu misika ya Admarc, iwo akumagulitsa chimanga cholemera makilogalamu 25 kwa munthu mmodzi pa mtengo wa K15, 000; mlingowu ndi theka la thumba lolemera makilogalamu 50. Izi zikutanthauza kuti makilogalamu 50 ndi K30, 000, koma iwo (Admarc) malire awo ndi makilogalamu 25.

Potengera ndi mabanja aku Malawi, banja limodzi limakhala ndi anthu osachepera asanu ndi awiri kotero thumba la makilogalamu 25 silokwanira kwenikweni.

Kwa mavenda pakadali pano, thumba lolemera makilogalamu 50 likugulitsidwa pakati pa K40,000 ndi K47,000 m’bomali komanso madera ena mdziko muno.

mavenda ndiwo akupha makwacha pogulitsa chimanga

Malingana ndi malipoti, anthu pafupifupi 4.5 miliyoni ndiamene ali pachiopsezo cha njala ku Malawi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *