Information and Technology Minister Gospel Kazako on Tuesday verbally attacked renowned Times TV presenter Brian Banda.
In a shocking tirade as the reporter tried to probe who is in charge of the country after President President Lazarus Chakwera, Kazako and two senior Minister told the public they were not aware of the arrest of ACB Director General Martha Chizuma.
Kazako did not answer the question but resorted to innuendos.
The Investigator transcribed the interview
Brian Banda: Timafuna tilandile omwe amalankhulila Boma ili anduna Gospel Kazako tikulandileni madzulo ano
Gospel Kazako: Zikomo Kwambiri
Brian Banda: Kunjaku Anthu akunena kuti iyii yakuphulikilani nkhaniyi, mumadziwa koma mwina mmangoyetsa madzi (you were testing the waters) nde yaphulika ndemufuna muoneke ngati kuti simmadziwa funso lofunikila kwambiri nali ndani akuonerela(Who is in control) ndani angadzuke lero ndi lero kulamula apolice kanjateni a Martha chizuma pomwe nonse kuphatikizilapo a president musakudziwa nchifukwa chake ndafunsa tili pabwino mdziko muno ndufuna muyankhe funsoli anduna (Who is in control) ndani akulamula ndani angalamule apolice kukachita zimenezi.
Gospel Kazako: nsanafike kumeneko
Brian Banda: Eya
Gospel Kazako: Kunena kuti chinthuchi chatiphulikila komanso kugwilitsa ntchito mau onena kuti anthu akuti anthu amatha kunena zinthu zosiyanasiyana
Brian Banda: iyayi ndimangofuna ndinene kuti mwina simukuziwa zimene anthu akunena kunjaku
Gospel Kazako: Ayi ayi chifukwa tikapanga choncho ndekuti tilakwisa
Brain banda: (mhm)
Gospel Kazako: ndofuna tisate nkhaniyi
Brian Banda: (mhm)
Gospel Kazako: ndofuna tisate nkani chifukwa anthu amatha kunena zinthu zambiri anthu amatha kunenana zinthu zokunyoza iweyo brian simene sizili zoona, a brian amagwilitsa ncthito certificate yam’bale wao anthu amanena zimenezi, abrian sadapiite ku school adalekeza form two, a biran izi a brian izi anthu amanena zinthu zosiyana siyana tinene kuti zinthuzi nzoona kuti mmagwilitsa ncthito pepala yam’bale wanu ayi
Brian Banda: Ndufuna tikambilane nkhani zeni zeni
Gospel Kazako: Ayi ayi nduziwa iyiso ndinkhani mwaimodzi yazokambilana
Brian Banda: ndufuna muyankhe Funso ililii ndani akuonerela (who is in Control)
Gospel Kazako: Iyinsoo ilimmodzi mwankhani yomwe tukambilana chifukwa iweee nde wabweresa nkhani yoti anthu akuti
Brian Banda: Iyayi iyayi
Gospel Kazako: ineso ndukupasa chisanzo kuti anthuso amanena kuti inu mulibe pepala la fomu folo (4) amangonena
Brian Banda: iyayi izo ndi nkhambakamwa chabe
Gospel Kazako: inde mongofananizila izonso zikhozakukhala chimodzimodzi kuti anthu akhoza kungonena zinthu nanga mufuna mukhulupilile zinthu zomwe anthu amakunenezelani zainu pokhapokha zikhale zoona tipitilize motere mofanana.
Brian Banda: Funso langa ndilakuti akuonelela ndindani (Who is in Control)
Gospel Kazako: ilo nde linali funso mukadandifunsa.
There has been mixed reaction from the public