MCP, UTM achotsana ma kholingo ku Blantyre

Anyamata otsatila zipani zomwe zili mgwirizano wa Tonse a Malawi Congress ndi UTM lachitatu sabata ino anakokana ma kholingo ndi kuswana ku malo aza malonda ku Chichiri mu mzinda wa Blantyre.

Akuluakulu azipanizi ati sizinakhale bwino koma aliyense akukankhila nzache kuti ndiye anayamba ntopola.

President Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake ku boma a Saulos Chilima anali ku mwambo wotsegulira chionetsero cha malonda pomwe achinyamatawa anali kugogadana ndi kuswana.

Wolankhulira UTM wati anyamata ena a MCP anathethemetsa  anyamata achipani chawo ndi zinthu za kuthwa pomwe amadikila kufika kwa atsogoleri.

Koma iwo sananene kuti achotsedwa chimbenene ndi angati.

Koma nduna ya za chitetezo yemwe ndi nkulu wa nfundo zoyendetsela chipani (Strategy) A Ken Zikhale Ng’oma akuti akuona ngati anthu azipani zina ndi omwe analowelelelapo kuti anthuwa aswane machaka.

Pakadali pano palibe yemwe wafotokoza kuti chinayambitsa mpungwe pungwe  ndi chani koma anthu azipani ziwirizi amanyozana kwambiri pa masamba a mchezo.

Malinga ndi ma video atuluka anyamata a UTM amayimba kuti Kongilesi inamunyoza Chilima itangowina. Izizi zimaoneka kuti sizinawasangalatse.

Mmodzi wa a katswiri andale wati kumenyana mwa ma supporters a UTM ndi MCP kukuonetsa kuti mgwirizano sukuyenda.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *