Miyala ya Nobium ku Mzimba afuna ayambe kukumba

Phindu lake ndi lotani?

Kingsley Jassi walemba izi pa tsamba lake la mchezo

Patatha zaka 8 boma likukambirana ndi company ya Globe Metals zotsekula mgodi wa Kanyika Niobium ku Mzimba, mbali ziwirizi zasayinira pangano la ntchitoyi. 

Nkofunika kudziwa kuti ngati dziko tipindulanji? 

Mgodiwu uzatulutsa niobium okwana matani 3 250 pa chaka, yemwe ndi mtapo othandizira kupanga ma battery a makono a lithium ion omwe amapezeka mu galimoto za magetsi, ma phone ndi zina. Pa mgodiwu pazatulukanso tantalum okwana matani 120 pa chaka. Tantalum amapangira ma capacitor a ma phone ndi zina. 

Niobium azizamugulitsa pa mtengo wosachepera $50 pa kilo pamene tantalum azizamugulitsa $260 pa kilo. Mitengoyi itha kumadzasintha koma izi ndi m’mene ziriri pano. Izi zikutanthauza kuti mgodiwu uzizabweretsa ndalama zakunja zokwana pafupi fupi $200 million pa chaka kwa za 20 ndipo pali kuthekera kuti mpaka zidzapitilira 30.

Boma lizizatengapo ma royalties omwe ndi 5% a malonda a pa chaka zomwe ndi $86.5 million ($4.3 million pa chaka) komanso msonkho wa 30% ya phindu lomwe kampani ya Globe Metals izapeze pa chaka womwe ukuyembekezeka kuzakwana $225 million ($11.1 million pa chaka). Kupatula apo, anthu a ku Kanyika azapindula ndi zitukuko za ndalama zokwana $10 million. Mitengo ya miyalayi ikazakwera ndekuti ndalamanso zizachuluka, ikazatsika nazonso zizachepa.

Kampaniyi ikuyembekezeka kumanga mgodiwu kwa zaka ziwiri kuyambira pomwe ntchitoyi izayambike ndipo ilowetsa mpamba wokwana $230 million. 

Osadzalira lira mtsogolomu kuti atibela. Izi ndi zina mwa zomwe ziri mu pangano lomwe boma lasayinirana ndi kampani ya Globe Metals.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *