Mikango ikufunika njira zolera, yachuluka

Mathews Malata

Bungwe la African Parks lonwe likuthandiza boma kusamalira nkhalango za Majete, Liwonde ndi Nkhotakota lati likulingalira zopempha boma kuti liyambe kugwiritsa ntchito ndondomeko “yakulera” pa mikango   yomwe ati yayamba kuchulukana maka mu nkhalango ya Majete. 

Mkulu wa African Parks kuno ku Malawi a Samuel Kamoto wati tsopano ku Majete kuli mikango makumi asanu ndipo wati tsopano zinafunika kuyamba kukonzekera kusamutsira ina mwa mikangoyi ku nkhalango zina zomwe zili zotetezedwa  bwino, kapena kugwiritsa ntchito njira zina zovomerezeka zomwe zingachepetse kuberekana kwa Mikangoyi. A Kamito ati pakadalipano palibe nkhalango yomwe ingathe kusunga mikango mosavuta kamba kuti kulibe mpanda oyenelera.

Koma mkulu wa nthambi yowona za nkhalango ndi nyama zakutchire bambo Brighton Kumchedwa wati pakadalipano boma silikufuna kugwiritsa ntchito njira ina iliyonse yochepetsera chiwerengero cha mikangoyi koma kuyisamutsira ku nkhalango zina. Iwo ati African Parks isade nkhawa ndi kusoweka kwa mipanda ku nkhalango zina kamba koti pali njira zambiri zomwe zingatsatidwe.

A Kumchedwa anatinso m’buyomu African Parks adapemphapo kuti ayambe njira za kulera pa Njobvu zomwe zachulukananso kwambiri koma adawakaniza pozindikira kuti pali nkhalango zambiri zomwe zikufunika zitabwereranso mchimake. Izi mwa zina ndizomwe zinapangitsa kuti Njobvu 263 azisamutsire ku malo osungirako nyama a Kasungu National Park.

Izi zakambidwa pa msonkhano omwe African Parks anakonza kudziwitsa anthu omwe amagwira nawo ntchito limodzi momwe ntchito zawo zayendera mchaka chathachi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *