Mpingo wa Katoloka wati ndalama ndi zopeleka zonse zilandile la Mulungu sabata ino azipeleka kwa anthu omwe akhuzidwa ndi cyclone Freddy.
Mkulu wa bungwe la ma Bishop a Katolika (Episcopal Conference of Malawi) Bishop George Tambala analengeza izi loweluka pomwe amapeleka thandizo kwa anthu akwa Mfumu Mpama mboma la Chiradzulu.
A Tambala anati mpingowu ndiwokhuzidwa ndi mavuto omwe cyclone wabweletsa ndipo akufuna kuthandizapo pochepetsa kuvutika kwa anthu.
Iwo anati mipingo ina ya Chikatolika ku Zambia monga wa Ndola nawonso wati upeleka zonse za mmbale kwa anthu okhuzidwawa.
Anthu oposa 360 anafa ndi madzi ndipo ena opitilila 500,000 akusowa pokhala.